Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU–NDANDANDA YA MISONKHANO NOVEMBER 2016

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NYIMBO YA SOLOMO 1-8

Msulami Ndi Chitsanzo Chabwino Kwambiri kwa Atumiki a Yehova

Msulami Ndi Chitsanzo Chabwino Kwambiri kwa Atumiki a Yehova

N’chifukwa chiyani tinganene kuti mtsikanayu ndi chitsanzo chabwino?

2:7; 4:12

  • Anali wanzeru ndipo anadikira mpaka atapeza chikondi chenicheni

  • Sankalola kuti anthu ena amukakamize kuti ayambe chibwenzi ndi munthu wina aliyense

  • Anali wodzichepetsa, wosakonda chuma komanso wodzisunga

  • Sanakopeke ndi zinthu ngati golide kapena mawu okopa achikondi

Dzifunseni kuti:

‘Kodi ndi khalidwe liti la mtsikanayu limene ndiyenera kuyesetsa kumutsanzira?’