Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MLALIKI 7-12

“Kumbukira Mlengi Wako Wamkulu Masiku a Unyamata Wako”

“Kumbukira Mlengi Wako Wamkulu Masiku a Unyamata Wako”

Muzikumbukira Mlengi Wanu Wamkulu pogwiritsa ntchito mphamvu zanu pomutumikira mudakali achinyamata

12:2-7

 • Achinyamata ambiri ndi athanzi komanso amphamvu moti akhoza kugwira ntchito zovuta

 • Achinyamata ayenera kugwiritsa ntchito nthawi komanso mphamvu zawo potumikira Mulungu asanayambe kukumana ndi mavuto obwera chifukwa cha ukalamba

Solomo anagwiritsa ntchito mawu andakatulo pofotokoza mavuto amene okalamba amakumana nawo

12:1, 13

 • Vesi 3: “Akazi oyang’ana pawindo azidzaona mdima”

  Kuvutika kuona

 • Vesi 4: “Ana onse aakazi azidzaimba nyimbo ndi mawu otsika”

  Kuvutika kumva

 • Vesi 5: Mawu enieni a vesili amanena za kuphulika kwa chipatso chinachake chimene munthu amadya kuti zakudya ziyambirenso kumukomera

  “Zakudya sizidzakoma”