Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu–Ndandanda ya Misonkhano  |  November 2016

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MLALIKI 1-6

Muzisangalala Chifukwa Chogwira Ntchito Mwakhama

Muzisangalala Chifukwa Chogwira Ntchito Mwakhama

Yehova amafuna kuti tizisangalala ndi ntchito yathu ndipo amatiphunzitsa mmene tingachitire zimenezi. Munthu akhoza kumasangalala ndi ntchito yake ngati amaigwira ndi maganizo oyenera.

Mukhoza kumasangalala ndi ntchito yanu . . .

3:13; 4:6

  • mukamaona ntchitoyo moyenera

  • mukamaganizira mmene ntchitoyo imathandizira anthu ena

  • mukamaigwira mwakhama, komabe mukaweruka muziyesetsa kuika maganizo pa banja lanu ndiponso kutumikira Yehova