Zimene Zili Papepala la Malangizoli

 

Ndime

Mawu Oyamba

 2

Chuma Chopezeka M’Mawu a Mulungu

 3

Kuphunzitsa Mwaluso mu Utumiki

 4

Moyo Wathu Wachikhristu

 5

Mawu Omaliza

 6

Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso

 7

Malangizo

 8

Kusunga Nthawi

 9

Woyang’anira Dera Akamachezera Mpingo

 10

Mlungu wa Msonkhano Wadera Kapena Wachigawo

 11

Mlungu wa Chikumbutso

 12

Woyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

 13

Tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

 14

Wogwirizanitsa Ntchito za Akulu

 15

Mlangizi Wothandiza

 16

Kalasi B

 17

Mavidiyo

 18

1. Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu uzichitika motsatira malangizo amene ali mu Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ndiponso amene ali papepala la malangizo lino. Ofalitsa onse akuyenera kulimbikitsidwa kuti alembetse n’cholinga choti azipatsidwa nkhani za ophunzira. Anthu enanso amene amasonkhana ndi mpingo nthawi zonse ndipo amatsatira mfundo zimene Baibulo limaphunzitsa komanso mfundo zachikhristu pa moyo wawo, angalembetse kuti azipatsidwa nkhani za ophunzirazi.​—be tsa. 282.

 2. Mawu Oyamba: Osapitirira 3 minitsi. Tiziyamba ndi nyimbo kenako pemphero. Ndiyeno tcheyamani wa msonkhanowu azifotokoza mwachidule zimene tiphunzire ndipo azitchula funso limodzi limene lili pa Pepala la Mayankho la Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu.

 3. Chuma Chopezeka M’Mawu a Mulungu:

  • Nkhani: 10 minitsi. Pa Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu pazikhala mutu komanso autilaini ya mfundo zazikulu ziwiri kapena zitatu. Nkhaniyi iyenera kuperekedwa kwa mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenerera. Tikamayamba buku latsopano la m’Baibulo, tizionera vidiyo. Ndiyeno wokamba nkhaniyo azisonyeza kugwirizana pakati pa vidiyoyo ndi mutu umene uli pa Ndandanda. Koma ayeneranso kuonetsetsa kuti wafotokoza mfundo zimene zaikidwa pandandandayo. Ayeneranso kugwiritsira ntchito zithunzi zimene zili pandandandayo, zomwe zimakonzedwa kuti zithandizire kumveketsa mfundo za m’nkhaniyo.

  • Kufufuza Mfundo Zothandiza: 8 minitsi. Nkhani ya mafunso ndi mayankho yopanda mawu oyamba ndiponso omaliza. Nkhaniyi izikambidwa ndi mkulu kapena mtumiki wothandiza  woyenerera. Iye ayenera kugawa bwino nthawi n’cholinga choti mfundo zonse 4 za m’nkhaniyi zifotokozedwe bwino mogwirizana ndi mpingowo. Iye ayenera kuonetsetsa kuti wafunsa mafunso onse m’nthawi imene wapatsidwa. Iye angasankhenso ngati zili zofunika kuwerenga mavesi onse amene aikidwa pa funso loyamba ndi lachiwiri. Anthu amene atchulidwa kuti ayankhe ayenera kufotokoza ndemanga zawo kwa nthawi yosapitirira masekondi 30.

  • Kuwerenga Baibulo: Osapitirira 4 minitsi. Nkhaniyi iperekedwe kwa m’bale. Ayenera kungowerenga mavesi amene wauzidwa popanda kunena mawu oyamba kapena omaliza. Tcheyamani ayenera kuthandiza munthuyo kuti amvetse zimene akuwerenga, awerenge molondola komanso mosadodoma, azisintha mawu, kupuma moyenera ndiponso kulankhula mwachibadwa.

  4. Kuphunzitsa Mwaluso mu Utumiki: Osapitirira 15 minitsi. Chigawo chimenechi cha msonkhano chakonzedwa kuti chizithandiza aliyense kuyeserera zimene angachite mu utumiki komanso kuwonjezera luso lolalikira ndi kuphunzitsa. Ophunzira azikamba nkhani zawo za ulendo woyamba ndiponso ulendo wobwereza mogwirizana ndi zitsanzo zimene zili pa tsamba loyamba la Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Ofalitsa angasankhe kuonetsa vidiyo kapena kugawira mwininyumba buku kapena kabuku zomwe zili pagawo la Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa. Pa Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu pali nthawi imene nkhani iliyonse ya ophunzira iyenera kukambidwa ndipo nthawi zina pandandandayi pangakhalenso malangizo ena owonjezera. Ophunzira sakuyenera kuwonjezera mfundo zina pa nkhani imene apatsidwa n’cholinga choti angomaliza nthawi yawo yonse. Kumbukirani kuti zitsanzo zina zokonzedwa bwino zikhoza kutha kutatsala miniti imodzi kapena maminitsi angapo. Akulu angapatsidwe nkhani za ophunzira, ngati pakufunika kutero.

  • Mavidiyo a Zimene Tinganene mu Utumiki: Tizionera mavidiyo a zimene tinganene mu utumiki kwa milungu yotsatizana mwezi uliwonse. Mavidiyowa azikhala a zitsanzo za ulendo oyamba, ulendo wobwereza woyamba, ndi ulendo wobwereza wachiwiri. Tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ndi amene azitsogolera mbali imeneyi.

  • Ulendo Woyamba: Nkhaniyi iperekedwe kwa m’bale kapena mlongo. Ngati yaperekedwa kwa mlongo, mwininyumba akhalenso mlongo ndipo ngati yaperekedwa kwa m’bale, mwininyumba akhalenso m’bale kapena munthu wa m’banja lake. Mwininkhani pamodzi ndi mwininyumba angasankhe kukhala pamipando kapena kuimirira, ndipo angapatsane moni wogwirizana ndi chikhalidwe cha kuderalo. Iwo agwiritse ntchito mfundo za pa chitsanzo cha zimene tinganene mu utumiki pokamba nkhani yawoyi.

  • Ulendo Wobwereza Woyamba: Nkhaniyi iperekedwe kwa m’bale kapena mlongo. Ngati yaperekedwa kwa mlongo, mwininyumba akhalenso mlongo ndipo ngati yaperekedwa kwa m’bale, mwininyumba akhalenso m’bale. (km 5/97 tsa. 2) Onse angakhale pamipando kapena kuimirira pamene akukamba nkhaniyi. Wophunzirayo asonyeze zoyenera kulankhula kwa munthu amene anasonyeza chidwi paulendo woyamba. Wophunzirayo agwiritse ntchito mfundo za pa chitsanzo cha zimene tinganene mu utumiki pokamba nkhaniyi.

  • Ulendo Wobwereza Wachiwiri: Nkhaniyi iperekedwe kwa m’bale kapena mlongo. Ngati yaperekedwa kwa mlongo, mwininyumba akhalenso mlongo ndipo ngati yaperekedwa kwa m’bale, mwininyumba akhalenso m’bale. (km 5/97 tsa. 2) Onse angakhale pamipando kapena kuimirira pamene akukamba nkhaniyi. Wophunzirayo asonyeze zoyenera kulankhula kwa munthu amene anasonyeza chidwi paulendo wobwereza woyamba. Wophunzirayo agwiritse ntchito mfundo za pa chitsanzo cha zimene tinganene mu utumiki pokamba nkhaniyi.

  • Phunziro la Baibulo: Nkhaniyi iperekedwe kwa m’bale kapena mlongo. Ngati yaperekedwa kwa mlongo, mwininyumba akhalenso mlongo ndipo ngati yaperekedwa kwa m’bale, mwininyumba akhalenso m’bale. (km 5/97 tsa. 2) Onse angakhale pamipando kapena kuimirira pamene akukamba nkhaniyi. Nkhaniyi izisonyeza phunziro la Baibulo lomwe layamba kale kuchitika. Palibe chifukwa chokhala ndi mawu oyamba kapena omaliza, pokhapokha ngati mutu wa phunziro  limene wophunzirayo wapatsidwa ukunena zimenezo. Sizofunika kuwerenga ndime zonse zimene mwapatsidwa, ngakhale kuti mungasankhe kuwerenga. Wokamba nkhaniyi akufunika kusonyeza luso labwino kwambiri lophunzitsa.

  • Nkhani: Nkhaniyi iziperekedwa kwa m’bale basi ndipo aziikamba yekha mofanana ndi nkhani zina zokambidwa pa mpingo.

  5. Moyo Wathu Wachikhristu: Nyimbo ikatha, 15 minitsi yotsatira ya chigawochi izikhala ndi nkhani imodzi kapena ziwiri zothandiza anthu kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu pamoyo wawo. Nkhanizi zingaperekedwe kwa akulu kapena atumiki othandiza oyenerera. Koma ngati ndi zofunika pampingo ziyenera kukambidwa ndi akulu okha.

  • Phunziro la Baibulo la Mpingo: 30 minitsi. Iperekedwe kwa mkulu woyenerera. (M’mipingo yomwe akulu ndi ochepa kwambiri, atumiki othandiza oyenerera angapatsidwe mbali imeneyi ngati pakufunika kutero.) Bungwe la akulu likuyenera kuunika luso lophunzitsa la mkulu aliyense kuti lisankhe akulu amene ali oyenerera kuchititsa Phunziro la Baibulo la Mpingo. Akulu amene angasankhidwewo akuyenera kuchititsa phunziroli mogwira mtima, kuthandiza omvera kuti atulutse mfundo zothandizadi pa malemba oyenerera, kuthandiza aliyense kuti aone mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’phunziroli pa moyo wake, ndipo sayenera kudya nthawi. Abale amene asankhidwa kuti azichititsa phunziroli akuyenera kuwerenga ndi kutsatira mfundo zimene gulu lafalitsa zokhudza mmene tingachititsire Phunziro la Nsanja ya Olonda. Ngati zili zotheka, mlungu uliwonse Phunziro la Baibulo la mpingo lizichititsidwa ndi m’bale wina ndipo m’bale winanso aziwerenga ndime, osati m’bale amene anawerenga mlungu wapita. Ngati tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu wanena kuti phunziroli lichitike mwachidule chifukwa cha nthawi, m’bale amene akuchititsa phunziroli azisankha yekha mmene angalichititsire mwachidule. Iye akhoza kusankha kuti ndime zina zisawerengedwe koma angofunsa mafunso.

  6. Mawu Omaliza: Osapitirira 3 minitsi. Tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu azibwereza mwachidule mfundo zothandiza zimene taphunzira pa msonkhanowo, kuphatikizapo funso la pa Pepala la Mayankho (lma). Azitchulanso funso limene tidzakambirane mlungu wotsatira, n’cholinga choti akonzekere. Ngati nthawi ilipo angatchule mayina a anthu amene apatsidwa nkhani mlungu wotsatira. Tcheyamani akhozanso kupereka zilengezo zofunika kapena kuwerenga makalata pa nthawi imeneyi. Zilengezo za nthawi zonse, monga zokhudza kulowa mu utumiki wa kumunda kapena kuyeretsa Nyumba ya Ufumu sizikuyenera kulengezedwa koma zizingoikidwa pabolodi la mpingo. Ngati zilengezo n’zambiri kapena kalata ndi yaitali ayenera kupeza nthawi kapena kupempha abale a nkhani pa gawo lakuti Moyo Wathu Wachikhristu, kuti azifupikitse. (Onani  ndime 5 ndi  9.) Msonkhanowu uzitha ndi nyimbo ndi pemphero.

 7. Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso: Kuyambira ndi mlungu wa January 7, 2019, tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu adzayamba kugwiritsa ntchito kabuku kakuti Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso poyamikira ndiponso kupereka malangizo kwa ophunzira. Mlungu woyambirira wa mwezi uliwonse, tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu azikambirana ndi omvera mutu umodzi wa kabuku ka Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso. Gawo lakuti “Zimene Inuyo Mwachita” la kabukuka lakonzedwa m’njira yakuti wophunzira aziligwiritsa ntchito osati kuti tcheyamani azilembapo.

  8. Malangizo: Wophunzira aliyense akamaliza nkhani yake, tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu azimuyamikira ndiponso kumupatsa malangizo kwa nthawi yosapitirira 1 miniti, ndipo malangizowo azichokera m’kabuku ka Kuphunzitsa. Akatchula wophunzira, tcheyamaniyo asatchule phunziro limene wapereka kwa wophunzirayo. Koma akamaliza, tcheyamaniyo ayenera kumuyamikira ndipo angatchule phunziro limene anamupatsa, kufotokoza mbali imene wachita  bwino kapena zimene ayenera kusintha ulendo wotsatira. Tcheyamani angasankhenso kuyamikira kapena kupereka malangizo pa mbali zina zokhudza mmene wophunzirayo wakambira nkhani yake ngati akuona kuti zingathandize wophunzirayo kapena omvera. Tcheyamani angaperekenso malangizo othandiza kwa wophunzira misonkhano ikatha kapena tsiku lina ndipo malangizowo ayenera kuchokera m’kabuku la Kuphunzitsa kapena buku la Sukulu ya Utumiki. Malangizowo angachokere pa phunziro limene wophunzirayo anapatsidwa kapena pa phunziro lina.​—Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya udindo wa woyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ndiponso udindo wa mlangizi wothandiza, onani  ndime 13 ndi  16.

    9. Kusunga Nthawi: Mbali iliyonse komanso ndemanga za tcheyamani zisapitirire nthawi yake. Nkhani za ophunzira ziziimitsidwa mwaluso nthawi yake ikatha. Ngati mbali zina zapitirira nthawi, mlangizi wothandiza azipereka malangizo kwa munthuyo pambali. Msonkhano wonse kuphatikiza nyimbo ndi pemphero zisapitirire ola limodzi ndi 45 minitsi.

 10. Woyang’anira Dera Akamachezera Mpingo: Woyang’anira dera akamachezera mpingo, mapulogalamu aziyenda mmene tasonyezera pa Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Koma nkhani yautumiki imene woyang’anira dera amakamba kwa 30 minitsi izilowa m’malo mwa Phunziro la Baibulo la Mpingo. Nkhani yautumikiyo isanayambe, tcheyamani ayenera kubwereza zimene taphunzira, kutchula pang’ono zimene tiphunzire mlungu wotsatira, kulengeza zinthu zofunika kenako kuitana woyang’anira derayo kuti adzakambe nkhani yake. Woyang’anira derayo akamaliza nkhani yake adzauza anthu kuti aimbe nyimbo yomaliza imene iye wasankha. Kalasi B ya m’chinenero cha mpingowo sikuyenera kuchitika pa mlungu umene woyang’anira dera akuchezera mpingo. Koma kagulu ka chinenero china kayenera kuchitabe misonkhano yake ngakhale kuti woyang’anira dera akuchezera mpingo umene umathandiza kaguluko. Koma pa nthawi imene woyang’anira dera akukamba nkhani yautumiki, kaguluko kakuyenera kumvetsera nkhaniyo.

 11. Mlungu wa Msonkhano Wadera Kapena Wachigawo: Ngati muli ndi msonkhano wadera kapena wachigawo, misonkhano yampingo ya mlunguwo siyenera kuchitika. Muyenera kuphunzira mfundo za pa misonkhano ya mpingoyo pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja kapena pophunzira panokha.

 12. Mlungu wa Chikumbutso: Misonkhano ya mpingo ya mkati mwa mlungu sikuyenera kuchitika ngati tsiku la Chikumbutso lilinso mkati mwa mlungu. Komabe, msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda ukuyenera kuchitika patsiku la Chikumbutso.

  13. Woyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu: Bungwe la akulu liyenera kusankha mkulu mmodzi kuti akhale woyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Iye azionetsetsa kuti msonkhanowu ukuchitika mwadongosolo komanso motsatira malangizo amene tafotokozawa. Ayeneranso kuchita zinthu mogwirizana ndi mlangizi wothandiza. Ndandanda ya Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya mwezi uliwonse ikangofika, iye ayenera kuperekeratu nkhani kwa ophunzira. (Onani  ndime 4.) Aliyense amene wapatsidwa nkhani ya ophunzira ayenera kudziwitsidwa kutatsala nthawi yosachepera milungu itatu kuti akambe nkhaniyo, pogwiritsa ntchito fomu ya Nkhani ya mu Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (S-89).

 14. Tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu: Mlungu uliwonse, mkulu azipemphedwa kukhala tcheyamani wa msonkhanowu. (Mipingo yomwe ili ndi akulu ochepa kwambiri, atumiki othandiza oyenerera angapemphedwe kukhala tcheyamani, ngati pakufunika kutero.) Tcheyamani azikamba mawu oyamba ndi omaliza, ndipo ndi amenenso ali ndi udindo wotsogolera pokambirana mavidiyo a zitsanzo za ulaliki komanso mavidiyo osonyeza phunziro latsopano m’kabuku la Kuphunzitsa. Aziitananso okamba nkhani zosiyanasiyana za msonkhanowu ndipo ngati akulu ndi ochepa, akhoza kumakambanso nkhani zina. Tcheyamani azilankhula mwachidule kwambiri nkhani iliyonse  ikatha komanso akamaitana wokamba nkhani yotsatira. Bungwe la akulu liyenera kusankha akulu oyenerera kuti azikhala matcheyamani ndipo azisinthanasinthana. Malinga ndi mmene zilili pa mpingopo, mwina woyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu angamakhale tcheyamani mobwerezabwereza kusiyana ndi akulu ena. Mkulu amene anavomerezedwa kuti azichititsa Phunziro la Baibulo la Mpingo ndiye kuti ndi woyeneranso kukhala tcheyamani wa msonkhanowu. Mkulu amene wasankhidwa kukhala tcheyamani ayenera kupereka malangizo achikondi komanso kuyamikira abale ndi alongo amene akamba nkhani za ophunzira. Tcheyamani ayenera kuonetsetsanso kuti misonkhano ikutha pa nthawi yake. (Onani  ndime 6 ndi  9.) Ngati tcheyamani angakonde komanso ngati kupulatifomu kuli malo okwanira, iye akhoza kuima pa maikofoni ena pambali kuti azilankhulirapo, amene akukamba nkhani yotsatira atafika kale pamaikofoni ake. Akhoza kusankhanso zokhaliratu kupulatifomuko pampando ataikanso tebulo lake kuti aziitana amene akukamba nkhani za ophunzira ndiponso kuwapatsa malangizo ali kupulatifomu komweko. Izi zingathandize kuti nthawi isawonongeke.

 15. Wogwirizanitsa Ntchito za Akulu: Wogwirizanitsa ntchito za akulu ndi amene azigawira anthu nkhani zonse kupatulapo za ophunzira. Pa akulu amene bungwe la akulu linawavomereza kuti azikhala matcheyamani, iye azisankhapo mkulu woti akhale tcheyamani mlungu uliwonse. Wogwirizanitsa ntchito za akulu limodzi ndi woyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu azionetsetsa kuti ndandanda ya misonkhano ya mwezi wonse yaikidwa pabolodi.

  16. Mlangizi Wothandiza: Ngati n’zotheka, sankhani mkulu amene amakamba bwino nkhani kuti akhale mlangizi wothandiza. Mlangiziyu azipereka malangizo kwa akulu ndi atumiki othandiza amene akamba nkhani zosiyanasiyana pamisonkhano yonse yampingo kaya ndi Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu, nkhani ya onse, Phunziro la Nsanja ya Olonda kapena Phunziro la Baibulo la Mpingo. (Onani  ndime 9.) Ngati mumpingomo muli akulu ambiri amene amakamba bwino nkhani, mungamasinthe mlangizi wothandiza chaka chilichonse. N’zosafunika kuti mlangizi wothandiza azipereka malangizo pamapeto a nkhani iliyonse.

 17. Kalasi B: Mipingo ingakhale ndi makalasi angapo mogwirizana ndi kuchuluka kwa ophunzira. Kalasi iliyonse ikhale ndi woyang’anira woyenerera ndipo ngati n’kotheka akhale mkulu. Mtumiki wothandiza woyenerera angagwiritsidwenso ntchito kukalasi B ngati zili zoyenera kutero. Bungwe la akulu liyenera kusankha m’bale kapena abale amene angakhale pa udindo umenewu, komanso ngati zili zofunika kuti abalewo azisinthanasinthana. Mlangiziyo ayenera kutsatira malangizo amene ali mu  ndime 8. Anthu ayenera kupemphedwa kuti apite kukalasi B pambuyo pa mbali yakuti Kufufuza Mfundo Zothandiza m’chigawo cha Chuma Chopezeka M’Mawu a Mulungu. Iwo ayenera kubwerera chigawo cha Kuphunzitsa Mwaluso mu Utumiki chikatha. Pakakhala mavidiyo a zitsanzo za ulaliki, abale ndi alongo amene ali kukalasi B ayenera kuonerera ndi kukambirana mavidiyowo kukalasi B komweko, ngati zili zotheka kutero. Mwina m’bale amene akutsogolera kalasi B angaonetse mavidiyowo pakompyuta kapena pachipangizo china cha m’manja.

 18. Mavidiyo: Pamsonkhanowu tizionera mavidiyo amene asankhidwa. Mavidiyo amene tizionera pamsonkhanowu azipezeka pa pulogalamu ya JW Library ndipo azitheka kuwatsegula pa zipangizo zosiyanasiyana. Nthawi zina, mavidiyo monga a zitsanzo za ulaliki tingawaonerenso pamsonkhano wokonzekera utumiki wakumunda, ngati anaonetsedwa kale pa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu.