4:16-18

Tayerekezani kuti mabanja awiri akukhala m’chinyumba chakutha komanso chakalekale. Banja limodzi likuoneka lankhawa kwambiri. Koma chodabwitsa n’choti banja linalo likuoneka losangalala. N’chifukwa chiyani mabanjawa ali osiyana choncho? Banja lachiwirili ndi losangalala chifuwa likudziwa kuti posachedwa lisamukira m’nyumba yabwino.

Ngakhale kuti “chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano,” anthu a Mulungu ali ndi chiyembekezo chomwe chimawathandiza kukhala osangalala. (Aroma 8:22) Mavuto omwe tikukumana nawowa, ngakhale kuti talimbana nawo kwa nthawi yaitali, ndi ‘akanthawi komanso opepuka’ tikawayerekezera ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. Choncho tikamaganizira madalitso omwe tidzapeze Ufumu ukadzayamba kulamulira padzikoli, timakhala osangalala komanso sitibwerera m’mbuyo.