Nyumba za Ufumu si nyumba wamba. Ndi malo athu olambirira omwe anaperekedwa kwa Yehova. Koma kodi tonse tingatani kuti tizithandiza nawo posamalira Nyumba ya Ufumu?

ONERANI VIDIYO YAKUTI KUSAMALIRA MALO ATHU OLAMBIRIRA KENAKO KAMBIRANANI MAFUNSO AWA:

  1. N’chifukwa chiyani timakhala ndi malo ochitira misonkhano?

  2. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamalira Nyumba ya Ufumu?

  3. Kodi kugwira nawo ntchito yosamalira malo athu olambirira kwakuthandizani bwanji?

  4. N’chifukwa chiyani kupewa ngozi n’kofunika? Nanga mwaona zinthu zotani m’vidiyoyi zomwe zingakuthandizeni kupewa ngozi?

  5. Kodi zopereka zathu zimathandiza bwanji kuti Yehova alemekezedwe?

ZIMENE NDIDZACHITE TIKAMADZASAMALIRANSO MALO ATHU OLAMBIRIRA