M’masiku otsiriza ano atumiki onse a Mulungu akukumana ndi mavuto aakulu okhala ngati munga. (2 Tim. 3:1) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timadalira Yehova kuti atithandize kupilira mavutowa? Onerani vidiyo yakuti “Maso a Anthu Akhungu Adzatsegulidwa” kuti mudziwe zimene Talita Alnashi ndi makolo ake anachita. Mukaonera vidiyoyi yankhani mafunso awa:

  • Kodi Talita akulimbana ndi vuto lanji?

  • Ndi malonjezo ati a m’Baibulo omwe athandiza Talita ndi makolo ake kuti asamakhale ndi nkhawa kwambiri?

  • Kodi Makolo a Talita anasonyeza bwanji kuti amadalira Yehova mwana wawo atangochitidwa kumene opaleshoni?

  • Kodi makolo a Talita amagwiritsa ntchito bwanji zinthu zomwe gulu lathu limatipatsa pothandiza mwana wawo kuti azikonda kwambiri Mulungu?

  • N’chiyani chikusonyeza kuti Talita akukula mwauzimu ngakhale kuti ali ndi “munga m’thupi”?

  • Kodi nkhani ya Talita yakulimbikitsani bwanji?