Palibe chimene chimawasangalatsa kwambiri makolo achikhristu kuposa kuona kuti mwana wawo ‘akudzikana yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo n’kumatsatira’ Yesu. (Maliko 8:34; 3 Yoh. 4) Kodi makolo angatani kuti athandize ana awo kuti azitsatira Yesu, adzipereke kwa Yehova komanso kubatizidwa? Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zingasonyeze kuti ana anu ndi okonzeka kubatizidwa?

Werengani, “Mawu kwa Makolo Achikhristu” patsamba 165-166 m’buku lakuti Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, kenako yankhani mafunso otsatirawa:

  1. Kodi kukhala wophunzira wa Khristu kumatanthauza chiyani?

  2. Kodi makolo ayenera kuwaphunzitsa chiyani ana awo?

  3. Kodi n’chifukwa chiyani ana ayenera kuyesetsa kutsatira mfundo za m’malemba otsatirawa kuti akhale oyenera kubatizidwa?