N’chifukwa chiyani atumwi anakodwa mumsampha woopa anthu?

14:29, 31

  • Ankadzidalira kwambiri. Mwachitsanzo Petulo ankaona kuti iyeyo adzakhalabe wokhulupirika kwa Yesu kuposa atumwi enawo

14:32, 37-41

  • Iwo analephera kukhalabe maso komanso anasiya kupemphera

Yesu ataukitsidwa, n’chiyani chinathandiza atumwi kuti asamaope anthu n’kumalalikirabe ngakhale kuti ankatsutsidwa?

13:9-13

  • Anamvera machenjezo a Yesu ndipo zotsatira zake analimba mtima pamene ankatsutsidwa komanso kuzunzidwa

  • Anadalira Yehova komanso anapemphera.​—Mac. 4:24, 29

Kodi ndi zochitika ziti zimene zingachititse kuti kulimba mtima kukhale kovuta?