CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Anaponya Zochuluka Kuposa Onse”: (10 min.)

  • Maliko 12:41, 42​—Yesu anaona mkazi wamasiye akuponya makobidi awiri aang’ono moponyamo zopereka (“moponyamo zopereka” “timakobidi tiwiri tating’ono” mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 12:41, 42, nwtsty)

  • Maliko 12:43​—Yesu anayamikira kwambiri zimene mayiyu anachita ndipo anafotokozera ophunzira ake (w97 10/15 16-17 ¶16-17)

  • Maliko 12:44​—Zimene mayiyu anapereka zinali zamtengo wapatali kwa Yehova (w97 10/15 17 ¶17; w87 12/1 30 ¶1; cl 185 ¶15)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Maliko 11:17​—N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti kachisi ndi “nyumba yopemphereramo mitundu yonse”? (“nyumba yopemphereramo mitundu yonse” mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 11:17, nwtsty)

  • Maliko 11:27, 28​—Kodi “zinthu” zomwe anthu otsutsa Yesuwa ankanena ndi ziti? (jy 244 ¶7)

  • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Maliko 12:13-27

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha zimene tinganene. Sonyezani mmene mungayankhire pa nkhani inayake yomwe anthu a m’gawo lanu amatsutsa kawirikawiri.

 • Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha zimene tinganene. Munthuyo wakufotokozerani kuti wachibale wake wamwalira posachedwapa.

 • Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU