Chilamulo cha Mose chinkanena kuti mwamuna akafuna kusiya mkazi wake ankafunika kukhala ndi kalata yothetsera ukwati. Zimenezi zinkathandiza kuti anthu asamangothetsa ukwati mwachisawawa. Komabe m’nthawi ya Yesu, atsogoleri achipembedzo ankachititsa kuti kuthetsa maukwati kuzikhala kosavuta. Amuna ankasiya akazi awo pazifukwa zosamveka. (“kalata yothetsa ukwati” mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 10:4, nwtsty, “wosiya mkazi wake” “wachita chigololo molakwira mkaziyo” mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 10:11, nwtsty) Yesu anasonyeza kuti Yehova ndi amene anayambitsa ukwati. (Maliko 10:2-12) Mwamuna ndi mkazi wake ankafunika kukhala “thupi limodzi” ndipo sankayenera kusiyana. Malinga ndi zimene Mateyu analemba pa nkhaniyi, chifukwa chimodzi chokha cha m’Malemba, chomwe chingachititse kuti ukwati uthe ndi “chigololo.”​—Mat. 19:9.

Masiku ano, anthu ambiri samaona ukwati ngati mmene Yesu ankauonera. Iwo amaona ngati mmene Afarisi ankauonera moti mavuto akabuka, amathamangira kuthetsa banja. Mosiyana ndi zimenezi, mabanja achikhristu amalemekeza zimene analonjeza patsiku la ukwati wawo ndipo amayesetsa kuthana ndi mavuto potsatira mfundo za m’Baibulo. Pambuyo poonera vidiyo yakuti, Chikondi ndi Ulemu Zimachititsa Banja Kukhala Logwirizana, yankhani mafunso otsatirawa:

  • Kodi mungatsatire bwanji mfundo ya pa Miyambo 15:1 m’banja lanu ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika?

  • Kodi kugwiritsa ntchito mfundo ya pa Miyambo 19:11 kungakuthandizeni bwanji kupewa mavuto m’banja?

  • Ngati banja lanu likuvutavuta, m’malo moganiza kuti ‘Mwinatu ndingolithetsa,’ kodi ndi mafunso ati amene muyenera kuwaganizira?

  • Kodi mfundo ya pa Mateyu 7:12, ingakuthandizeni bwanji kukhala mwamuna kapena mkazi wabwino?