Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 44-48

Leka ‘Kufunafuna Zinthu Zazikulu’

Leka ‘Kufunafuna Zinthu Zazikulu’

45:2-5

Zikuoneka kuti Baruki anali munthu wophunzira kwambiri ndipo ankagwira ntchito m’nyumba ya mfumu. Ngakhale kuti ankalambira Yehova komanso ankathandiza Yeremiya mokhulupirika, nthawi ina anachita zinthu mosaganiza bwino. Iye anayamba ‘kufunafuna zinthu zazikulu,’ mwina ankafuna kutchuka kapena chuma. Choncho anafunika kusintha maganizo kuti apulumuke pamene Yerusalemu ankawonongedwa.