• Nyimbo Na. 23 ndi Pemphero

 • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Tizidalira Yehova Kuti Tikhale Olimba Mtima”: (10 min.)

  • Sal. 27:1-3—Tikamakumbukira kuti Yehova ndiye kuwala kwathu timakhala olimba mtima (w12 7/15 22-23 ndime 3-6)

  • Sal. 27:4—Chikhulupiriro chathu chimalimba kwambiri tikamakonda kulambira koona (w12 7/15 24 ndime 7)

  • Sal. 27:10—Yehova ndi wokonzeka kuthandiza atumiki ake ngakhale anthu ena atawasiya (w12 7/15 24 ndime 9-10)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Sal. 26:6—Mofanana ndi Davide, kodi tingazungulire bwanji guwa la nsembe la Yehova? (w06 5/15 19 ndime 10)

  • Sal. 32:8—Kodi timapindula bwanji Yehova akamatipatsa nzeru? (w09 6/1 5 ndime 3)

  • Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Masalimo 32:1–33:8

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) kt—Werengani lemba pogwiritsa ntchito foni kapena chipangizo china chamakono.

 • Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingapemphere munthu amene timam’patsa magazini mwezi uliwonse kuti tiziphunzira naye Baibulo. Muonetseni vidiyo yakuti Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji? kuchokera pa Laibulale ya JW.

 • Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) jl Phunziro 9—Sonyezani mwachidule wophunzirayo mmene angagwiritsire nchito Laibulale ya JW pokonzekera misonkhano.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 130

 • Zofunika pampingo: (15 min.) Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo. Nkhani.

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) cl mutu 31 ndime 1-12

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 16 ndi Pemphero