Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  May 2016

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 11-18

Ndani Angakhale Mlendo M’chihema cha Yehova?

Ndani Angakhale Mlendo M’chihema cha Yehova?

Kuti munthu akhale mlendo m’chihema cha Yehova ayenera kukhala mnzake wa Mulungu ndipo ayenera kumukhulupirira ndi kumumvera. Salimo 15 limafotokoza zimene Yehova amafuna kuti mabwenzi ake azichita.

MLENDO WA YEHOVA AYENERA . . .

  • kukhala ndi mtima wosagawanika

  • kunena zoona, ngakhale mumtima mwake

  • kulemekeza atumiki a Yehova anzake

  • kukwaniritsa zimene walonjeza ngakhale ataona kuti n’zovuta kuchita zimenezo

  • kuthandiza anthu ovutika popanda kuyembekezera kuti amubwezere

MLENDO WA YEHOVA AMAPEWA . . .

  • miseche ndi bodza

  • kuchitira anzake zoipa

  • kudyera masuku pamutu Akhristu anzake

  • kugwirizana ndi anthu amene satumikira kapena kumvera Yehova

  • kulandira ziphuphu