Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Mmene Tingagwiritsire Ntchito Laibulale ya JW

Mmene Tingagwiritsire Ntchito Laibulale ya JW

POPHUNZIRA:

  • Mungawerenge Baibulo ndi lemba la tsiku.

  • Mungawerenge Buku Lapachaka, magazini ndi mabuku ena ambiri. Gwiritsani ntchito kachizindikiro kokuthandizani kukumbukira

  • Mukhoza kukonzekera misonkhano yampingo ndiponso kuchekenera mayankho

  • Mungaonere mavidiyo

PAMISONKHANO:

  • Mungawerenge malemba omwe wokamba nkhani akutchula. Ngati mukufuna kuti muonenso lemba lomwe munaliwerenga kale, dinani pomwe pali kachizindikiro ka wotchi kapena timadontho titatu kumapeto kwa chipangizo chanu

  • M’malo mobweretsa mabuku ambirimbiri kumisonkhano, mungathe kuimba nyimbo ndi kutsatira mbali zosiyanasiyana za misonkhano pogwiritsa ntchito mabuku omwe ali m’chipangizo chanu. Laibulale ya JW ili ndi nyimbo zatsopano zomwe m’buku la nyimbo mulibe

MU UTUMIKI:

  • Mungasonyeze munthu wachidwi buku kapena magazini omwe akupezeka pa Laibulale ya JW. Mungamuthandizenso kupanga dawunilodi pulogalamuyi ndiponso mabuku pogwiritsa ntchito chipangizo chake

  • Mungagwiritse ntchito kachizindikiro kofufuzira aka pofuna kupeza vesi linalake

  • Mungaonetse munthu vidiyo. Ngati amene mukuwalalikira ali ndi ana, mungawasonyeze kavidiyo kamodzi ka Khalani Bwenzi la Yehova. Kapenanso mungawasonyeze kavidiyo kakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? pofuna kuwathandiza kuti akhale ndi chidwi chofuna kuphunzira Baibulo. Ngati mwakumana ndi munthu woyankhula chinenero china, musonyezeni vidiyo ya m’chinenero chakecho

  • Sonyezani munthu lemba la chinenero china m’Baibulo limene munapanga dawunilodi. Kuti muchite zimenezi, tsegulani lembalo ndipo dinani panambala ya vesilo kenako dinani kachizindikiro ka Baibulo