Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  May 2016

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 38-42

Yehova Amasangalala Tikamapempherera Ena

Yehova Amasangalala Tikamapempherera Ena

Yehova ankayembekezera kuti Yobu apempherere Elifazi, Bilidadi ndi Zofari

42:7-10

  • Yehova anauza Elifazi, Bilidadi ndi Zofari kuti apite kwa Yobu kukadziperekera nsembe

  • Yehova ankayembekezera kuti Yobu awapempherere

  • Yobu atapempherera anzakewo Yehova anamudalitsa

Yehova anadalitsa Yobu chifukwa anali wokhulupirika komanso wopirira

42:10-17

  • Yehova anathetsa mavuto onse a Yobu n’kumupatsanso moyo wathanzi

  • Yobu anatonthozedwa kwambiri ndi anzake komanso achibale

  • Yehova anapatsanso Yobu chuma chochuluka, kuwirikiza kawiri chuma chomwe anali nacho poyamba

  • Yobu ndi mkazi wake anaberekanso ana 10

  • Yobu anakhalanso ndi moyo kwa zaka zina 140 ndipo anaona mibadwo 4 ya banja lake