Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  May 2016

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mumagwiritsa Ntchito Laibulale ya JW?

Kodi Mumagwiritsa Ntchito Laibulale ya JW?

Laibulale ya JW ndi yaulere ndipo ingakuthandizeni kupanga dawunilodi zinthu monga Baibulo, magazini, mavidiyo ndi zinthu zina zongomvetsera kuti muzizigwiritsa ntchito mufoni, tabuleti kapena pakompyuta.

KODI MUNGAIPEZE BWANJI?: Pitani pa Intaneti pamalo amene pamapezeka pulogalamu yopangira dawunilodi mapulogalamu osiyanasiyana. Kenako mungapange dawunilodi Laibulale ya JW, n’kuisunga m’chipangizo chanu. Mukatero tsegulani pulogalamuyi ndi kupanga dawunilodi mabuku kapenanso zinthu zina zomwe mukufuna. Ngati kunyumba kwanu kulibe netiweki ya intaneti, mukhoza kupita ku Nyumba ya Ufumu, kunyumba kwa mnzanu, kapenanso mungakalipire kumalo ena kumene kuli netiweki ya intaneti m’dera lanu. Mukapanga dawunilodi mabuku n’kuwasunga m’chipangizo chanu, simufunikiranso kupita pa intaneti kuti muwawerenge. Komabe popeza kuti nthawi ndi nthawi papulogalamuyi amaikapo zinthu zina zatsopano, muyenera kumapita pa intaneti kuti muone zomwe aikapo.

KODI INGAKUTHANDIZENI BWANJI? Mungathe kugwiritsa ntchito Laibulale ya JW pophunzira Baibulo panokha komanso pamisonkhano yampingo. Ndi yothandizanso kwambiri mu utumiki makamaka polalikira mwamwayi ngakhale kwa anthu omwe safuna kuwalalikira.