CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Mmene Tingasonyezere Chikondi Chachikhristu”: (10 min.)

  • Aroma 12:10​—Muzikonda Akhristu anzanu (it-1 55)

  • Aroma 12:17-19​—Munthu akakulakwirani, musamabwezere (w09 10/15 8 ¶3; w07 7/1 24-25 ¶12-13)

  • Aroma 12:20, 21​—Gonjetsani choipa pochita chabwino (w12 11/15 29 ¶13)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Aroma 12:1​—Kodi vesi limeneli likutanthauza chiyani? (lvs 76-77 ¶5-6)

  • Aroma 13:1​—Kodi “olamulira amene alipowa ali m’malo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu” m’njira yotani? (w08 6/15 31 ¶4)

  • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Aroma 13:1-14 (th phunziro 10)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Kugwiritsa Ntchito Mafunso, kenako kambiranani phunziro 3 m’kabuku ka Kuphunzitsa.

 • Nkhani: (Osapitirira 5 min.) w11 9/1 21-22​—Mutu: N’chifukwa Chiyani Akhristu Amafunikabe Kulipira Misonkho Ngakhale Kuti Ndalamazo Zingagwiritsidwe Ntchito pa Zinthu Zosagwirizana ndi Malemba? (th phunziro 3)

MOYO WATHU WACHIKHRISTU