Anthu amachita chidwi ndi zomwe aona ndipo zimawathandiza kumvetsa komanso kukumbukira zomwe aphunzira. Yehova, monga Mlangizi Wamkulu, wakhala akuphunzitsa anthu pogwiritsa ntchito zinthu zooneka. (Gen. 15:5; Yer. 18:1-6) Yesu nayenso yemwe anali Mphunzitsi Waluso, ankaphunzitsa anthu pogwiritsa ntchito njira imeneyi. (Mat. 18:2-6; 22:19-21) Masiku ano timagwiritsa ntchito mavidiyo monga njira imodzi yophunzitsira anthu ndipo njirayi ndi yothandiza kwambiri. Kodi nanunso mumagwiritsa ntchito mavidiyo mukamaphunzira Baibulo ndi anthu?

Panakonzedwa mavidiyo 10 omwe cholinga chake n’kutithandiza tikamaphunzira ndi anthu pogwiritsa ntchito kabuku ka Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu. Mitu ya mavidiyowa ndi yogwirizana ndi funso linalake lomwe likupezeka m’kabukuka. Pazipangizo zamakono, kabukuka kakonzedwanso kuti kazikhala ndi malinki otithandiza kudziwa malo omwe tikufunika kuonetsa vidiyo. Tilinso ndi mavidiyo ena omwe ali ndi mfundo zofanana ndi zomwe zikupezeka m’zinthu zomwe timagwiritsa ntchito pophunzitsa.

Kodi mukuphunzira mfundo ya m’Baibulo imene wophunzira wanu angavutike kuimvetsa? Kodi wophunzira wanuyo akukumana ndi mayesero enaake? Ngati ndi choncho, mungafufuze pa jw.org® kapena pa JW Broadcasting® kuti mupeze vidiyo yomwe ingamuthandize. Mwina mungaonere limodzi vidiyoyo kenako n’kukambirana.

Mavidiyo atsopano amatuluka mwezi ulionse. Mukamaonera mavidiyo amenewa muziganizira mmene mungawagwiritsire ntchito pophunzira ndi anthu.