2:14-16

Aliyense ayenera kupitirizabe kukula mwauzimu n’kufika pomaona zinthu mmene Yehova amazionera. (Aef. 4:23, 24) Kuti zimenezi zitheke tiyenera kumaphunzira Mawu a Mulungu, kukhala ndi zolinga zauzimu komanso kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.

Kodi ubwenzi wanu ndi Yehova wakula bwanji panopa mukayerekezera ndi mmene unalili chaka chapitachi, zaka 10 zapitazo kapena mutangobatizidwa kumene?