CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Pitirizani Kukhala Maso M’masiku Otsiriza Ano(10 min.)

  • Mat. 24:12​—Kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo kwachititsa kuti chikondi cha anthu ambiri chizirale (it-2 279 ¶6)

  • Mat. 24:39​—Anthu ena akutanganidwa ndi zinthu zatsiku ndi tsiku ndipo zawachititsa kuti azilephera kutumikira Mulungu bwinobwino (w99 11/15 19 ¶5)

  • Mat. 24:44​—Ambuye adzabwera pa nthawi imene anthu sakuyembekezera (jy 259 ¶4)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Mat. 24:8​—Kodi n’kutheka kuti mawu a Yesuwa akutanthauza chiyani? (Mfundo zimene ndikuphunzira za “chiyambi cha masautso” pa Mat. 24:8, nwtsty)

  • Mat. 24:20​—N’chifukwa chiyani Yesu analankhula mawu amenewa? (Mfundo zimene ndikuphunzira za “m’nyengo ya chisanu,” “pa tsiku la sabata” pa Mat. 24:20, nwtsty)

  • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mat. 24:1-22

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire pa nkhani inayake yomwe anthu a m’gawo lanu amatsutsa kawirikawiri.

 • Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza woyamba. Munthu amene munacheza naye ulendo wapita simunamupeze pakhomo koma mwapeza wachibale wake.

 • Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU