CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Khalanibe Maso”: (10 min.)

  • Mat. 25:1-6​—Anamwali 5 ochenjera komanso anamwali 5 opusa anatuluka kukachingamira mkwati

  • Mat. 25:7-10​—Anamwali opusa anali atachokapo pamene mkwati ankafika

  • Mat. 25:11, 12​—Anamwali ochenjera okha ndi amene analoledwa kulowa nawo m’nyumba imene munali phwando laukwati

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Mat. 25:31-33​—Fotokozani fanizo la nkhosa ndi mbuzi (w15 3/15 27 ¶7)

  • Mat. 25:40​—Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife anzawo a abale ake a Khristu? (w09 10/15 16 ¶16-18)

  • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mat. 25:1-23

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha zimene tinganene. Muitanireni ku mwambo wa Chikumbutso.

 • Ulendo Wobwereza Wachitatu: (Osapitirira 3 min.) Sankhani lemba lililonse ndipo gawirani buku kapena kabuku kamene timagwiritsa ntchito pophunzira ndi anthu.

 • Nkhani: (Osapitirira 6 min.) w15 3/15 27 ¶7-10​—Mutu: Kodi Fanizo la Nkhosa ndi Mbuzi Likusonyeza Bwanji Kufunika Kwa Ntchito Yolalikira?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 85

 • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Azikonzekera”: (10 min.) Nkhani yokambirana. Kenako, onetsani ndi kukambirana vidiyo yosonyeza wofalitsa akuthandiza munthu amene amaphunzira naye Baibulo kuti azikonzekera phunzirolo. Pemphani omvera kuti afotokoze njira zina zimene amaona kuti n’zothandiza pophunzitsa ophunzira awo kuti azikonzekera phunziro la Baibulo.

 • Tidzalandire Bwino Alendo: (5 min.) Nkhani yochokera mu Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya March 2016. Fotokozani zinthu zosangalatsa zomwe zinachitika pa nthawi ya Chikumbutso cha 2017. Kumbutsani abale ndi alongo dongosolo lomwe lakonzedwa lokhudza koimika magalimoto, kulowa komanso kutuluka pamalo omwe tikuchitira chikumbutso komanso zinthu zina zokhudza mwambowu womwe udzachitike pa 31 March.

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 15 ¶29-36 komanso bokosi patsamba 167

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 79 ndi Pemphero