Ngakhale kuti Akhristu satsatira Chilamulo cha Mose, malamulo ake awiri aakulu kwambiri omwe ndi kukonda Mulungu komanso anzathu, amasonyezabe zimene Yehova amafuna kuti tizichita. (Mat. 22:37-39) Chikondi chimenechi sichimangoyamba chokha mwa munthu. Timafunika kuchikulitsa. Ndiye tingachite bwanji zimenezi? Njira yofunika kwambiri imene tingachitire zimenezi ndi kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. Tikamaphunzira zimene Malemba amanena zokhudza makhalidwe a Mulungu, timayamba kuona “ubwino wa Yehova.” (Sal. 27:4) Izi zimachititsa kuti tiyambe kumukonda kwambiri komanso timayamba kuganiza mofanana naye. Zimenezi zimatilimbikitsa kutsatira malamulo ake, kuphatikizapo lamulo losonyeza ena chikondi chopanda dyera. (Yoh. 13:34, 35; 1 Yoh. 5:3) Tsopano onani mfundo zitatu zomwe zingatithandize kuti tizisangalala kwambiri tikamawerenga Baibulo.

  • Muziyerekezera kuti mukumva komanso kuona zimene zikuchitikazo m’maganizo mwanu. Muziyerekezera kuti munalipo pa nthawiyo. Kodi mukuona komanso kumva chiyani, nanga pamalopo pakumveka kafungo kotani? Kodi anthu omwe ali pamalowo akumva bwanji?

  • Muzisinthasintha njira zowerengera. Mungagwiritse ntchito njira ngati izi: Mungamawerenge mokweza kapena kumatsatira pamene mukumvetsera Baibulo longomvetsera. Mungamawerenge zokhudza munthu winawake wotchulidwa m’Baibulo kapena mfundo zokhudza nkhani inayake m’malo mowerenga machaputala motsatira ndondomeko yake. Mwachitsanzo, mungagwiritse ntchito Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu mutu 4 kapena 16 kuti muwerenge nkhani zokhudza Yesu. Mungamawerenge chaputala chonse chomwe pachokera lemba la tsiku limenelo. Mukhozanso kumawerenga Baibulo motsatira nthawi imene mabuku ake analembedwa.

  • Muziwerenga n’cholinga choti mumvetse. Kuwerenga chaputala chimodzi pa tsiku n’cholinga choti mumvetse komanso kusinkhasinkha zimene mukuwerengazo n’kopindulitsa kwambiri, kusiyana ndi kuwerenga machaputala ambirimbiri n’cholinga choti mumalize kuwerenga Baibulo lonse. Muziganizira malo amene nkhaniyo inachitikira komanso mbali zosiyanasiyana za nkhaniyo. Mukhozanso kugwiritsa ntchito mapu ndiponso malifalensi omwe ali mu danga la pakati m’Baibulo lanu. Mungachitenso bwino kumafufuza mfundo zomwe simunazimvetse. Ngati n’zotheka, muzisinkhasinkha zimene mwawerengazo kwa nthawi yofanana ndi imene mwawerenga Baibulo.