Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  March 2017

March 6-12

YEREMIYA 1-4

March 6-12
 • Nyimbo Na. 23 ndi Pemphero

 • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Ine Ndili ndi Iwe Kuti Ndikulanditse”: (10 min.)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Yer. 2:13, 18—Kodi Aisiraeli osakhulupirika anachita zinthu ziwiri ziti zomwe zinali zoipa? (w07 3/15 9 ¶8)

  • Yer. 4:10—Kodi mawu oti Yehova ‘anapusitsa’ anthu ake akutanthauza chiyani? (w07 3/15 9 ¶4)

  • Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Yer. 4:1-10

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Kukonzekera Ulaliki wa Mwezi Uno: (15 min.) Kukambirana Zitsanzo za Ulaliki. Pambuyo poonetsa vidiyo ya chitsanzo cha ulaliki iliyonse, kambiranani mfundo zikuluzikulu za m’vidiyoyo.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 149

 • Zimene Gulu Lathu Lachita: (7 min.) Onetsani vidiyo ya Zimene Gulu Lathu Lachita ya March.

 • Ntchito Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa 18 March: (8 min.) Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki yochokera mu Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya February 2016, tsamba 8. Perekani kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso kwa aliyense n’kukambirana mfundo zake. Fotokozani zimene mpingo wakonza pofuna kuti mudzathe kugawira timapepalati kwa anthu onse a m’gawo lanu.

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 19 ¶1-16

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 74 ndi Pemphero