Yeremiya anapatsidwa ntchito yochenjeza Ayuda kuti adzawonongedwa chifukwa chakuti anaiwala Mulungu wawo Yehova. (Yer. 13:25) Kodi n’chiyani chinachititsa kuti zinthu zifike poipa chonchi ku Yuda? Mabanja achiisiraeli anali atasiya kukonda Yehova. Zikuoneka kuti amuna amene anali ndi banja sankatsatira malangizo amene Yehova anapereka pa Deuteronomo 6:5-7.

Masiku ano mabanja amene amakonda kwambiri Yehova amathandiza kuti zinthu ziziyenda bwino mumpingo. Amuna angathandize anthu a m’banja lawo kuti azikumbukira Yehova pochita nawo Kulambira kwa Pabanja nthawi zonse komanso m’njira yabwino. (Sal. 22:27) Pambuyo poonetsa vidiyo yakuti Mawu Awa . . . Azikhala Pamtima Pako”Kucheza ndi Mabanja, kambiranani mafunso awa:

  • Kodi mabanja ena athana bwanji ndi mavuto amene ambiri amakumana nawo pochita Kulambira kwa Pabanja?

  • Kodi timapindula bwanji tikamachita Kulambira kwa Pabanja nthawi zonse komanso m’njira yabwino?

  • Kodi ndi mavuto ati amene mumakumana nawo okhudza Kulambira kwa Pabanja, nanga mungawathetse bwanji?