Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  March 2016

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | ESITERE 6-10

Esitere Anasonyeza Kuti Sanali Wodzikonda

Esitere Anasonyeza Kuti Sanali Wodzikonda
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

Esitere anasonyeza kuti ndi wolimba mtima komanso wosadzikonda poteteza anthu a Yehova

8:3-5, 9

  • Moyo wa Esitere ndi Moredekai sunali pangozi. Koma lamulo la Hamani loti Ayuda onse aphedwe n’kuti likulengezedwa mu ufumu wonse wa Ahasiwero

  • Esitere anaika moyo wake pangozi pokaonekeranso pamaso pa mfumu asanaitanidwe. Iye analira n’kupempha mfumuyo kuti isinthe lamulo limene Hamani anakhazikitsa

  • Malamulo operekedwa m’dzina la mfumu sankasinthidwa. Choncho mfumuyo inapatsa mphamvu Esitere ndi Moredekai kuti apange lamulo latsopano

Yehova anathandiza anthu ake kuti apambane

8:10-14, 17

  • Lamulo lachiwiri linalengezedwa ndipo linapatsa Ayuda mphamvu yoti adziteteze

  • Anthu okwera pa mahatchi anatumizidwa m’zigawo zonse za ufumuwo kuti akakonzekeretse Ayuda kumenya nkhondo

  • Anthu ambiri anaona kuti Yehova amakonda anthu ake ndipo ena anayamba kutsatira chipembedzo cha Ayuda