Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu–Ndandanda ya Misonkhano  |  March 2016

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 11-15

Yobu Sankakayikira Kuti Akufa Adzauka

Yobu Sankakayikira Kuti Akufa Adzauka

Yobu anasonyeza kuti ankakhulupirira kuti Mulungu adzamuukitsa

14:7-9, 13-15

  • Yobu anagwiritsa ntchito chitsanzo cha mtengo, mwina wa maolivi, pofuna kusonyeza chikhulupiriro chimene anali nacho chakuti Mulungu angathe kumuukitsa

  • Mizu ya mtengo wa maolivi imakhala yambiri komanso imakafika patali. Zimenezi zimachititsa kuti chitsa chake chiziphukirabe ngakhale thunthu lake litadulidwa

  • Ngakhale kutachita chilala mpaka chitsa cha mtengowu kuuma, kukagwa mvula, nthambi zina zimaphukiranso kuchokera ku mizu yake