Yobu anakhalabe wokhulupirika ngakhale kuti chuma chake chonse chinatha, ana ake onse anafa komanso anadwala kwambiri. Koma Satana anayesetsabe kuchita zinthu zoipa n’cholinga choti Yobu akhumudwe n’kusiya kutumikira Yehova. Tsiku lina kunyumba kwa Yobu kunabwera “anzake” atatu. Anzakewo atafika, anachita zinthu zosonyeza kuti akumumvera chisoni. Iwo anakhala naye limodzi masiku 7, popanda kumuyankhula chilichonse. Pambuyo pake anayamba kuyankhula zinthu zosonyeza kuti Yobu anali wolakwa.

Yobu anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova ngakhale kuti panali zofooketsa zambiri

6:3; 7:16; 9:20-22; 10:1, 12

  • Chifukwa chowawidwa mtima kwambiri ndi mavuto, Yobu anayamba kuona zinthu molakwika. Anaganiza kuti Mulungu analibe nazo ntchito ngakhale kuti iye anayesetsa kukhala wokhulupirika

  • Chifukwa chokhumudwa, Yobu sanaganizire kuti pangakhale zifukwa zina zimene zikanachititsa kuti avutike

  • Ngakhale kuti anali ndi chisoni kwambiri, Yobu anauza anzake amene ankamuimba mlanduwo kuti iye ankakondabe kwambiri Yehova