Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  March 2016

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 1-5

Yobu Anakhalabe Wokhulupirika Pamene Ankayesedwa

Yobu Anakhalabe Wokhulupirika Pamene Ankayesedwa

Yobu ankakhala m’dziko la Uzi pa nthawi imene Aisiraeli anali akapolo ku Iguputo. Ngakhale kuti sanali Mwisiraeli, iye ankalambira Yehova. Anali ndi banja lalikulu ndipo anali wolemera kwambiri. Iye anali munthu wolemekezeka, ankaweruza milandu mwachilungamo komanso ankathandiza anthu osauka. Yobu anali wokhulupirika kwa Mulungu.

Zimene Yobu anachita zinasonyeza kuti ankakonda kwambiri Yehova

1:8-11, 22; 2:2-5

  • Satana ankadziwa kuti Yobu ndi munthu wokhulupirika. Iye sanakane zoti Yobu ankamvera Yehova, koma anakayikira ngati ankatumikira Yehova ndi zolinga zabwino

  • Satana ananena kuti Yobu ankatumikira Yehova chifukwa cha zinthu zabwino zimene ankamuchitira

  • Pofuna kutsimikizira kuti zimene ankanenazo zinali zabodza, Yehova analola Satana kuti ayese Yobu. Choncho, Satana anachititsa kuti Yobu akumane ndi mavuto ambiri pamoyo wake

  • Ngakhale kuti Yobu anapitiriza kukhala wokhulupirika kwa Yehova, Satana anayamba kukayikira ngati anthu angamatumikire Mulungu mokhulupirika pamene akukumana ndi mavuto

  • Yobu sanachimwe kapena kunena kuti Mulungu amachita zoipa