Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu ali pamwambo wokumbukira imfa ya Khristu ku Germany

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU March 2016

Zitsanzo za Ulaliki

Zimene tinganene pogawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso mu 2016. Gwiritsani ntchito zitsanzozi kuti mukonze ulaliki wanuwanu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Esitere Anasonyeza Kuti Sanali Wodzikonda

Iye analimba mtima n’kuika moyo wake pangozi pothandiza Moredekai kukhazikitsa lamulo loteteza Ayuda kuti asaphedwe (Esitere 6-10)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Kukonza Ulaliki Wanuwanu wa Magazini

Gwiritsani ntchito mfundo zimenezi kukonza ulaliki wa Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tidzalandire Bwino Alendo

Kodi tidzathandize bwanji alendo komanso anthu amene anasiya kusonkhana kuti adzakhale omasuka pa Chikumbutso?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yobu Anakhalabe Wokhulupirika Pamene Ankayesedwa

Yobu ankaona kuti kukonda Yehova ndi kofunika kwambiri. (Job 1-5)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yobu Anasonyeza Kukhumudwa Kwake

Yobu anayamba kuganiza zolakwika chifukwa cha kuchuluka kwa mavuto komanso zinthu zofooketsa zimene anthu ankalankhula. koma sanasiye kukonda Yehova Mulungu. (Job 6-10)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yobu Sankakayikira Kuti Akufa Adzauka

Iye ankakhulupirira kuti Yehova adzabwezeretsa moyo wake ngati mmene chimachitira chitsa cha mtengo wa maolivi chomwe chimatha kuphukiranso. (Yobu 11-15)

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Imfa ya Yesu Inathandiza Kuti Akufa Adzaukitsidwe

Dipo limene Yehova anapereka linathandiza kuti akufa adzakhalenso ndi moyo. Nthawi imeneyo anthu sadzafanso ndipo okondedwa athu amene anamwalira adzaukitsidwa.