4:24-31

Mtumwi Paulo anafotokoza nkhani ‘yophiphiritsira’ pofuna kusonyeza kuti pangano latsopano ndi lofunika kwambiri kusiyana ndi pangano lachilamulo. Yesu komanso Akhristu odzozedwa adzathandiza anthu onse kuti amasuke ku uchimo, imfa komanso zopweteka.​—Yes. 25:8, 9.

 

HAGARA, KAPOLO WAMKAZI

Akuimira mtundu wa Isiraeli womwe unkatsatira Chilamulo ndipo likulu lawo linali ku Yerusalemu

“ANA” A HAGARA

Akuimira Ayuda (amene analonjeza kuti adzatsatira Chilamulo) omwe anakana komanso kuzunza Yesu

AKAPOLO A PANGANO LACHILAMULO

Chilamulo chinkakumbutsa Aisiraeli kuti anali akapolo a uchimo

SARA, YEMWE ANALI MFULU

Akuimira Yerusalemu wakumwamba, yemwe ndi mbali yakumwamba ya gulu la Mulungu

“ANA” A SARA

Akuimira Khristu ndi Akhristu odzozedwa okwana 144,000

PANGANO LATSOPANO LIMAPEREKA UFULU

Kukhulupirira nsembe ya Khristu kumabweretsa ufulu womwe umamasula munthu ku ukapolo wa Chilamulo