CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Nkhani ‘Yophiphiritsira’ Yomwe ndi Yofunika Kwambiri kwa Ife”: (10 min.)

  • Agal. 4:24, 25​—Hagara ankaimira mtundu wa Isiraeli womwe unkatsatira Chilamulo (it-1 1018 ¶2)

  • Agal. 4:26, 27​—Sara ankaimira ‘Yerusalemu wakumwamba,’ yemwe ndi mbali yakumwamba ya gulu la Yehova (w14 10/15 10 ¶11)

  • Agal. 4:28-31​—Anthu omvera adzadalitsidwa kudzera mwa “ana” a Yerusalemu wakumwamba

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Agal. 4:6​—Kodi mawu achiheberi kapena achialamu akuti abba, amatanthauza chiyani? (w09 4/1 13)

  • Agal. 6:17​—Kodi n’kutheka kuti mtumwi Paulo ankatanthauza chiyani ponena kuti thupi lake linali ndi “zipsera za chizindikiro cha kapolo wa Yesu?” (w10 11/1 15)

  • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Agal. 4:1-20 (th phunziro 10)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Kufotokoza Bwino Malemba, kenako kambiranani phunziro 6 m’kabuku ka Kuphunzitsa.

 • Nkhani: (Osapitirira 5 min.) w12 3/15 30-31​—Mutu: N’chifukwa Chiyani Akhristu Ayenera Kupeweratu Kuwonera Zolaula? (th phunziro 13)

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 110

 • Zofunika Pampingo: (8 min.)

 • Zimene Gulu Lathu Lachita: (7 min.) Onetsani vidiyo ya Zimene Gulu Lathu Lachita ya June.

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 38

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 147 ndi Pemphero