Kodi nthawi zina mumaona kuti ntchito yolalikira ndi yovuta? Ambirife tikhoza kuyankha kuti inde. Izi zili choncho mwina chifukwa chakuti anthu ena a m’gawo lathu alibe chidwi, ena amatsutsa komanso mwina ifeyo timaopa kulankhula ndi anthu osawadziwa. Zimenezi zikhoza kuchititsa kuti tisamasangalale. Komatu timalambira Mulungu wachimwemwe ndipo iye amafuna kuti tizimutumikira mosangalala. (Sal. 100:2; 1 Tim. 1:11) Kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene zingachititse kuti tizisangalala tikamagwira ntchito yolalikira?

Choyamba, uthenga wathu umathandiza kuti anthu aziyembekezera zabwino m’tsogolo. Popeza kuti anthu m’dzikoli alibe chiyembekezo, ifeyo timawauza “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” (Yes. 52:7) Komatu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umatithandizanso ifeyo kuti tizisangalala. Choncho tisanapite kukalalikira, tiziganizira madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse padzikoli.

Chachiwiri, uthenga umene timalalikira umathandiza kuti anthu asiye makhalidwe oipa ndi kuyamba kukonda Mulungu. Izi zimawachititsa kuti aziyembekezera kudzalandira moyo wosatha. (Yes. 48:17, 18; Aroma 1:16) Ntchito imene timagwira ndi yopulumutsa anthu. Choncho, tiziyesetsa kufufuza anthu amene akufuna kudzapulumuka ngakhale kuti ena safuna kuti tiwathandize.​—Mat. 10:11-14.

Chachitatu komanso chofunika kwambiri n’chakuti ntchito yathu yolalikira imalemekeza Yehova. Iye amaiona kuti ndi yofunika kwambiri. (Yes. 43:10; Aheb. 6:10) Yehova amatipatsanso mzimu woyera kuti tikwanitse kugwira ntchitoyi. Choncho tizimupempha kuti azitithandiza kukhala ndi khalidwe la mzimuwo, lomwe ndi chimwemwe. (Agal. 5:22) Iye angatithandize kuti tisakhale ndi nkhawa komanso kuti tizilalikira molimba mtima. (Mac. 4:31) Ndiyeno, kaya anthu m’gawo lathu amatitsutsa kapena kulandira uthenga wathu, tidzapitirizabe kukhala osangalala.​—Ezek. 3:3.

Kodi ndi khalidwe liti limene mukufuna kuti muzisonyeza mukakhala mu utumiki? Kodi mungatani kuti muzisangalala?

ONERANI VIDIYO YAKUTI KUSINKHASINKHA KUNGATITHANDIZE KUKHALA WOSANGALALA, KENAKO YAKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • N’chifukwa chiyani nthawi zonse tiyenera kukhala ndi nthawi yophunzira Mawu a Mulungu mwakhama ngakhale kuti timalalikira maola ambiri mwezi uliwonse?

  • Kodi tingatsanzire Mariya m’njira ziti?

  • Kodi inuyo mumaona kuti nthawi yabwino yosinkhasinkha Mawu a Mulungu ndi iti?

  • Kodi n’chiyani chimakusangalatsani mukamalalikira uthenga wabwino?