Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  June 2017

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZEKIELI 1-5

Ezekieli Anasangalala Kulengeza Uthenga wa Mulungu

Ezekieli Anasangalala Kulengeza Uthenga wa Mulungu

M’masomphenya, Yehova anapatsa Ezekieli mpukutu n’kumuuza kuti adye. Kodi zimenezi zinkatanthauza chiyani?

2:9–3:2

  • Ezekieli ankafunika kuwerenga komanso kumvetsa bwino uthenga wa Mulungu. Kusinkhasinkha zimene ankawerenga mumpukutu kunachititsa kuti uthenga wake umufike pamtima ndipo izi zinamulimbikitsa kuti aziuza ena

3:3

  • Ezekieli ankamva kuti mpukutuwo unkatsekemera chifukwa choti anasangalala ndi ntchito imene anapatsidwa

Kodi kuphunzira Baibulo ndi kusinkhasinkha kungandithandize bwanji?

 

Kodi ndingatani kuti ndizisangalala ndi ntchito yolalikira?