Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  June 2017

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 51–52

Nthawi Zonse Mawu a Yehova Amakwaniritsidwa

Nthawi Zonse Mawu a Yehova Amakwaniritsidwa

Yehova ananeneratu molondola zinthu zam’tsogolo

Msilikali wachiperisiya

“Nolani mivi yanu”

51:11, 28

  • Amedi ndi Aperisi anali akatswiri oponya mivi ndipo ankadalira kwambiri mauta. Iwo ankanola mivi yawo kuti akabaya izilowa mkati kwambiri

“Amuna amphamvu a ku Babulo asiya kumenya nkhondo”

51:30

  • Mbiri ya Nabonidus imati: “Magulu a nkhondo a Koresi analowa m’Babulo popanda kumenya nkhondo.” Izi zikutanthauza kuti Koresi analowa mumzinda wa Babulo popanda wolimbana naye ndipo n’zogwirizana ndi zimene ulosi wa Yeremiya unanena

Mbiri ya Nabonidus

“Babulo adzakhala milu yamiyala [ndiponso] bwinja mpaka kalekale”

51:37, 62

  • Kuyambira m’chaka cha 539 B.C.E., ulemerero wa Babulo unayamba kuchepa. Alekizanda Wamkulu ankafuna kuti mzinda wa Babulo ukhale likulu la ulamuliro wake, koma pasanapite nthawi anamwalira. Chikhristu chitangoyamba kumene, mtumwi Petulo ankafika ku Babulo chifukwa kunali Ayuda ena omwe ankakhala kumeneko. Koma pofika m’zaka za m’ma 300 C.E., mzindawo unawonongedwa ndipo sunakhaleponso

Kodi kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo kungandithandize bwanji?

 

Kodi ndingaphunzitse ena chiyani zokhudza ulosiwu?