Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  June 2017

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mumakhulupirira Kwambiri Zimene Yehova Analonjeza?

Kodi Mumakhulupirira Kwambiri Zimene Yehova Analonjeza?

Yoswa komanso Solomo anatsimikiza kuti mawu onse amene Yehova ananena anakwaniritsidwa. (Yos. 23:14; 1 Maf. 8:56) Zimene anthu awiriwa ananena zingatithandize kulimbitsa chikhulupiriro chathu.​—2 Akor. 13:1; Tito 1:2.

Kodi Yehova anakwaniritsa bwanji malonjezo ake m’nthawi ya Yoswa? Limodzi ndi banja lanu, onerani vidiyo yakuti ‘Palibe Ngakhale Mawu Amodzi Omwe Sanakwaniritsidwe.’ Kenako yankhani mafunso otsatirawa: (1) Kodi tingatsanzire bwanji chikhulupiriro cha Rahabi? (Aheb. 11:31; Yak. 2:24-26) (2) Kodi chitsanzo cha Akani chikusonyeza bwanji kuti kusamvera kumabweretsa mavuto? (3) Kodi n’chifukwa chiyani amuna a ku Gibeoni, ngakhale kuti anali odziwa kumenya nkhondo, ananamiza Yoswa n’kuchita pangano la mtendere ndi Aisiraeli? (4) Kodi mawu a Yehova anakwaniritsidwa bwanji pamene mafumu 5 a Aamori ankaopseza Aisiraeli? (Yos. 10:5-14) (5) Kodi Yehova anakuthandizani bwanji inuyo chifukwa choika Ufumu ndi chilungamo chake pamalo oyamba?​—Mat. 6:33.

Tikamaganizira zonse zimene Yehova anachita, zimene akuchita panopa komanso zimene adzachite m’tsogolo, chikhulupiriro chathu pa malonjezo ake chimalimba kwambiri.​—Aroma 8:31, 32.

Kodi muli ndi chikhulupiriro ngati cha Yoswa?