Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  June 2017

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tizitsatira Mfundo za Makhalidwe Abwino za Yehova

Tizitsatira Mfundo za Makhalidwe Abwino za Yehova

Yehova Mulungu anakhazikitsa mfundo za makhalidwe abwino zoti anthu azitsatira. Mwachitsanzo, iye ananena kuti banja ndi mgwirizano wapakati pa mwamuna ndi mkazi basi. (Mat. 19:4-6, 9) Yehova amadana ndi khalidwe lachiwerewere la mtundu uliwonse. (1 Akor. 6:9, 10) Amaperekanso malangizo pa nkhani ya zovala ndi kudzikongoletsa, zomwe zimasiyanitsa anthu ake ndi ena.​—Deut. 22:5; 1 Tim. 2:9, 10.

Masiku ano anthu ambiri m’dzikoli safuna kutsatira mfundo za Yehova. (Aroma 1:18-32) Iwo amangotsatira maganizo a anthu ena pa nkhani ya kuvala ndi kudzikongoletsa komanso khalidwe lawo. Ambiri amadzitamandira chifukwa chochita zoipa ndipo amanyoza anthu amene amatsatira mfundo zosiyana ndi zawo.​—1 Pet. 4:3, 4.

Popeza kuti ndife Mboni za Yehova, tiyenera kutsatira mfundo zake za makhalidwe abwino. (Aroma 12:9) Tingachite zimenezi pouza anthu ena zimene Yehova amafuna. Komanso ifeyo tisasiye kutsatira mfundozo. Mwachitsanzo, tikamasankha masitayilo a zovala komanso kudzikongoletsa, tingadzifunse kuti: ‘Kodi zimene ndasankhazi zikugwirizana ndi mfundo za Yehova kapena za dzikoli? Kodi mmene ndimavalira komanso mmene ndimadzikongoletsera zimasonyeza kuti ndine Mkhristu?’ Tikamasankha mafilimu kapena mapulogalamu a pa TV, tingadzifunse kuti: ‘Kodi Yehova angasangalale ndi pulogalamuyi? Kodi ikulimbikitsa mfundo za ndani? Kodi zosangalatsa zimene ndimakonda sizingawononge makhalidwe anga? (Sal. 101:3) Kodi sizingakhumudwitse anthu a m’banja langa kapena anthu ena?’​—1 Akor. 10:31-33.

Kodi n’chifukwa chiyani n’kofunika kuti tizitsatira mfundo za Yehova za makhalidwe abwino? Posachedwapa Yesu Khristu adzawononga anthu oipa komanso adzachotsa zoipa zonse. (Ezek. 9:4-7) Amene adzapulumuke ndi okhawo omwe amachita zimene Mulungu amafuna. (1 Yoh. 2:15-17) Choncho tiyeni tipitirize kutsatira mfundo za Yehova za makhalidwe abwino kuti anthu akaona khalidwe lathu labwino azilemekeza Mulungu.​—1 Pet. 2:11, 12.

Kodi zimene ndimasankha pa nkhani ya zovala ndi kudzikongoletsa zimasonyeza kuti ndili ndi khalidwe lotani?

ONERANI VIDIYO YAKUTI KHALANI BWENZI LA YEHOVA​—MWAMUNA MMODZI, MKAZI MMODZI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • N’chifukwa chiyani kutsatira mfundo za Yehova n’kofunika kwambiri?

  • N’chifukwa chiyani makolo ayenera kuyamba kuphunzitsa ana awo adakali aang’ono mfundo za Yehova za makhalidwe abwino?

  • Kodi ana ndi akuluakulu omwe, angathandize bwanji anthu kuti apindule ndi ubwino wa Mulungu?