Masomphenya a Ezekieli anakwaniritsidwa koyamba pamene Yerusalemu anawonongedwa. Nanga kodi adzakwaniritsidwa bwanji m’tsogolomu?

9:1, 2

  • Munthu wokhala ndi kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki ndi zolembera akuimira Yesu Khristu

  • Amuna 6 okhala ndi zida zophwanyira akuimira gulu lankhondo lakumwamba lotsogoleredwa ndi Khristu

9:3-7

  • A khamu lalikulu adzalembedwa chizindikiro akadzaweruzidwa kuti ndi nkhosa pa chisautso chachikulu

Kodi ndizichita chiyani kuti ndidzalembedwe chizindikiro chosonyeza kuti ndine woyenera kupulumuka?