Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Mlongo akuphunzira Baibulo komanso kusinkhasinkha

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU June 2017

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za ulaliki za Galamukani! komanso kuphunzitsa choonadi chokhudza mphatso ya moyo. Gwiritsani ntchito zitsanzozi kuti mupange ulaliki wanuwanu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Nthawi Zonse Mawu a Yehova Amakwaniritsidwa

Ulosi wa Yeremiya wonena kuti Babulo adzawonongedwa unakwaniritsidwa.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mumakhulupirira Kwambiri Zimene Yehova Analonjeza?

Yoswa anatsimikiza kuti palibe mawu ngakhale amodzi amene Yehova ananena kwa Aisiraeli omwe sanakwaniritsidwe. Kodi tingatani kuti tizikhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Mtima Wodikira Umatithandiza Kuti Tipirire

Kodi n’chiyani chinathandiza kuti Yeremiya apirire ngakhale kuti anakumana ndi mavuto aakulu? Nanga kodi tingakonzekere bwanji mavuto amene tingakumane nawo m’tsogolo?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Ezekieli Anasangalala Kulengeza Uthenga wa Mulungu

M’masomphenya, Yehova anapatsa Ezekieli mpukutu kuti adye. Kodi zimenezi zinkatanthauza chiyani?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzisangalala Mukamalalikira Uthenga Wabwino

Nthawi zina kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kukhoza kuoneka kosasangalatsa, koma Mulungu amafuna kuti tizisangalala tikamamutumikira. Kodi tingatani kuti tizisangalala tikamagwira ntchito yathu yolalikira?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Kodi Mudzalembedwa Chizindikiro Choti Ndinu Woyenera Kupulumuka?

Masomphenya a Ezekieli anakwaniritsidwa koyamba pamene Yerusalemu anawonongedwa. Nanga kodi kukwaniritsidwa kwa ulosiwu masiku ano kukutikhudza bwanji?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tizitsatira Mfundo za Makhalidwe Abwino za Yehova

Tiziyesetsa kutsatira mfundo za makhalidwe abwino za Yehova Mulungu. Kodi tingachita bwanji zimenezi? N’chifukwa chiyani zili zofunika?