Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu Mu Utumiki—Kugwiritsa Ntchito Mavidiyo Pophunzitsa

Kuwonjezera Luso Lathu Mu Utumiki—Kugwiritsa Ntchito Mavidiyo Pophunzitsa

N’CHIFUKWA CHIYANI KUCHITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA?:

Mavidiyo akhoza kufika munthu pamtima chifukwa munthuyo amawona ndi kumva zomwe zikuchitika. Amathandizanso kuti chidwi cha munthu chisathe komanso kuti asaiwale zomwe waphunzira. Ndipotu Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pogwiritsa ntchito zinthu zooneka pophunzitsa.—Mac. 10:9-16; Chiv. 1:1.

Mavidiyo akuti, Kodi Mulungu Ali ndi Dzina?, Kodi Mlembi Wamkulu wa Baibulo Ndani? komanso Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona? amathandiza kwambiri kuti munthu amvetse bwino mfundo za m’mitu 2 ndi 3 ya m’kabuku ka Uthenga Wabwino. Mavidiyo akuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?, Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji? ndi Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? amalimbikitsa anthu kuti aziphunzira Baibulo komanso kuti azisonkhana. Palinso mavidiyo ena omwe mungagwiritse ntchito pophunzitsa anthu.—km 5/13 3.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Muzipangiratu dawunilodi vidiyo imene mukufuna kukaonetsa mwininyumba

  • Muzikonzekera funso loti mwininyumba akapeze yankho lake akakaonera vidiyoyo

  • Muzionera limodzi vidiyoyo

  • Muzikambirana mfundo zofunika zomwe mwapeza

TAYESANI KUCHITA IZI:

  • Onani kuseri kwa kapepala kamodzi, kenako mumusonyeze pomwe pali kachidindo kothandiza munthu kutsekula vidiyo yakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?

  • Onetsani vidiyo yakuti, Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona? kenako gawirani kabuku ka Uthenga Wabwino, ndipo mungagwiritse nchito mfundo za mu phunziro 3.