Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu–Ndandanda ya Misonkhano  |  June 2016

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 52-59

“Umutulire Yehova Nkhawa Zako”

“Umutulire Yehova Nkhawa Zako”

Davide anakumana ndi mayesero ambiri othetsa nzeru. Pamene Salimo 55 linkalembedwa, n’kuti atakumana ndi zinthu monga . . .

  • Kunyozedwa

  • Kuzunzidwa

  • Kudziimba Mlandu

  • Mavuto a M’banja

  • Kudwala

  • Kuukiridwa

Davide anakwanitsa kupirira mavuto ake ngakhale kuti mavutowo ankaoneka ngati amukulira. Iye analemba malangizo othandiza anthu omwe amaona kuti n’zovuta kupirira mayesero omwe akukumana nawo. Anati: “Umutulire Yehova nkhawa zako.”

Kodi tingagwiritse ntchito bwanji vesili masiku ano?

55:22

  1. Tizipemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima tikakumana ndi vuto linalake komanso ngati tikuda nkhawa ndi zinazake

  2. Tizifufuza malangizo opezeka m’Mawu a Yehova komanso omwe gulu lake limapereka

  3. Tiziyesetsa kupeza mfundo za m’Baibulo zomwe zingatithandize kuchepetsa mavuto omwe takumana nawo