Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU–NDANDANDA YA MISONKHANO JUNE 2016

June 27–July 3

MASALIMO 52-59

June 27–July 3
 • Nyimbo Na. 38 ndi Pemphero

 • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Umutulire Yehova Nkhawa Zako”: (10 min.)

  • Sal. 55:2, 4, 5, 16-18—Nthawi zina Davide ankavutika ndi nkhawa (w06 6/1 11 ndime 5; w96 4/30 27 ndime 2)

  • Sal. 55:12-14—Davide anaukiridwa ndi mwana wake komanso mnzake yemwe ankamukhulupirira (w96 4/1 30 ndime 1; w12 4/15 9 ndime 5)

  • Sal. 55:22—Davide anasonyeza kuti ankakhulupirira kuti Yehova amuthandiza (w06 6/1 11 ndime 6; w99 3/15 22-23)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Sal. 56:8—Kodi mawu akuti, “Sungani misozi yanga m’thumba lanu lachikopa,” akutanthauza chiyani? (w09 6/1 28 ndime 5; w08 10/1 26 ndime 3)

  • Sal. 59:1, 2—Kodi zimene Davide anakumana nazo zikutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya pemphero? (w08 3/15 14 ndime 13)

  • Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Sal. 52:1–53:6

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gawirani kapepala kamodzi. Mufotokozereni za kachidindo kamene kali patsamba lomaliza.

 • Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Chitani chitsanzo chosonyeza ulendo wobwereza kwa munthu amene analandira kapepala.

 • Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) fg phunziro 3 ndime 2-3—Pomaliza mufotokozereni za vidiyo ya pa jw.org yakuti, Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 56

 • Zofunika pampingo: (7 min.)

 • Mulungu Ndiye Mthandizi Wanga”: (8 min.) Nkhani yokambirana. Onetsetsani kuti mafunso a m’nkhaniyi ayankhidwa ndi anthu ochuluka n’cholinga choti aliyense apindule ndi zimene abale ndi alongo awo anakumana nazo. (Aroma 1:12) Limbikitsani ofalitsa kuti azigwiritsa ntchito Buku Lofufuzira Nkhani pofuna kupeza mfundo za m’Mawu a Mulungu akakumana ndi mavuto.

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 1 ndime 1-13

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 121 ndi Pemphero