Anthu omwe akufuna kukhala nzika za Ufumu wa Mulungu ayenera kuyesetsa kuphunzira zokhudza Ufumuwu ndiponso zimene wachita kale panopo. N’chifukwa chiyani ayenera kuchita zimenezi? N’chifukwa chakuti chikhulupiriro chawo chidzakhala cholimba podziwa kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira komanso zimenezi zidzawathandiza kuti aziuza ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Sal. 48:12, 13) Mukamaonera vidiyo yakuti Ufumu wa Mulungu Wakwanitsa Zaka 100 Ndipo Ukulamulirabe, mupeze mayankho a mafunso awa:

  1. N’chifukwa chiyani tinganene kuti “Sewero la Pakanema la Chilengedwe” linathandiza anthu omwe analionera?

  2. Kodi ankagwiritsa ntchito bwanji wailesi pouza anthu uthenga wabwino?

  3. Kodi ndi njira zina ziti zomwe anagwiritsa ntchito pouza anthu uthenga wabwino, nanga zotsatira zake zinali zotani?

  4. Kodi ntchito yophunzitsa anthu utumiki yasintha bwanji m’zaka zapitazi?

  5. Kodi ndi mfundo zothandiza ziti zomwe ophunzira a Sukulu ya Giliyadi anaphunzitsidwa?

  6. Kodi misonkhano ikuluikulu yathandiza bwanji kuphunzitsa anthu a Yehova?

  7. Kodi n’chiyani chimene chimakutsimikizirani kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira?

  8. Kodi timasonyeza bwanji kuti tili kumbali ya Ufumu wa Mulungu?