Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  June 2016

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 45-51

Yehova Sadzasiya Anthu Amtima Wosweka

Yehova Sadzasiya Anthu Amtima Wosweka

Davide analemba Salimo 51 pambuyo poti mneneri Natani waulula tchimo lachigololo lomwe Davideyo anachita ndi Bateseba. Zimenezi zinkamusautsa mumtima ndipo anadzichepetsa n’kuvomereza tchimo lakelo.—2 Sam. 12:1-14.

Ngakhale kuti Davide anachimwa, Mulungu anali wokonzeka kumukhululukira

51:3, 4, 8-12, 17

  • Asanavomereze ndiponso kulapa tchimo lakelo, ankasowa mtendere

  • Davide anavutika mumtima atadziwa kuti wakhumudwitsa Mulungu, mofanana ndi mmene munthu amamvera mafupa ake akaphwanyidwa

  • Iye ankafunitsitsa kukonzanso ubwenzi wake ndi Mulungu komanso kukhululukidwa n’cholinga choti azisangalala ngati poyamba

  • Iye anapempha Yehova modzichepetsa kuti amuthandize kukhala ndi mtima womvera

  • Ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova amukhululukira