Mkulu akuphunzitsa m’bale wachinyamata ntchito zapampingo

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU July 2019

Zimene Tinganene

Zitsanzo za ulaliki zofotokoza chimene chimachititsa kuti tizivutika komanso mmene mavuto adzathere.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Vulani Umunthu Wakale N’kuvala Umunthu Watsopano

Kungochokera pamene tinabatizidwa, timayenera kupitiriza kuvula umunthu wakale n’kuvala umunthu watsopano.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Pitirizani Kutonthozana ndi Kulimbikitsana”

Tonsefe tingathe kulimbikitsa ena. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Wosamvera Malamulo Adzaonekera

Chinsinsi cha ‘wosamvera malamulo’ chafotokozedwa m’chaputala 2 cha kalata yachiwiri yopita kwa Atesalonika.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yesetsani Kuti Mukhale Oyang’anira

Abale obatizidwa, kuphatikizapo omwe adakali achinyamata, ayenera kumayesetsa kuchita zinthu zomwe zingawathandize kuti adzakhale pa udindo m’tsogolo. Koma kodi angachite bwanji zimenezi?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Mungaphunzire Zambiri Kuchokera kwa Achikulire

Ngati mwangoikidwa kumene kukhala mtumiki wothandiza kapena mkulu, kodi mungasonyeze bwanji kuti mumalemekeza Akhristu omwe amadziwa zambiri, nanga mungatani kuti muziphunzira kuchokera kwa iwo?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Kukhala Wodzipereka kwa Mulungu N’kofunika Kuposa Chuma

N’chifukwa chiyani tinganene kuti tingakhale osangalala kwambiri ngati titakhala wodzipereka kwa Mulungu m’malo mofunafuna chuma?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kudzipereka kwa Mulungu N’kofunika Kuposa Kuchita Masewera

Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zomwe zingathandize Akhristu kuti asamalole kuti masewera aziwalepheretsa kuchita zinthu zauzimu?