9:62

Kuti munthu amene ankalima ndi pulawo alime mizere yowongoka, sankafunika kuyang’ana zinthu zakumbuyo. Mofanana ndi zimenezi, Mkhristu sayenera kusokonezedwa ndi zinthu za m’dzikoli zimene anazisiya.​—Afil. 3:13.

Tikakumana ndi mavuto n’zosavuta kuyamba kuganiza za nthawi imene tinali tisanaphunzire choonadi n’kumanena kuti, ‘Koma kale likanati lizibwerera!’ Munthu akamachita zimenezi amakhala akungoganizira za zinthu zabwino zimene ankapeza koma saganizira za mavuto amene ankakumana nawo. Izi ndi zomwe Aisiraeli anachita atachoka ku Iguputo. (Num. 11:5, 6) Tikamaganizira kwambiri zinthu za m’mbuyo, tikhoza kukopeka n’kuyamba kuchita zimene tinasiya. Choncho ndi nzeru kumaganizira madalitso amene tikupeza panopo, komanso amene tidzapeze m’tsogolo mu Ufumu wa Mulungu.​—2 Akor. 4:16-18.