12:6, 7

Kodi n’chiyani chomwe chinachititsa Yesu kunena mawu a pa Luka 12:6, 7? Mu vesi 4, Yesu anauza ophunzira ake kuti asamaope anthu omwe amawatsutsa kapena amene amafuna kuwapha. Yesu ankafuna kuti ophunzira ake akhale okonzeka kuti asadzavutike akadzayamba kutsutsidwa. Iye anawatsimikizira kuti Yehova amaona kuti atumiki ake ndi amtengo wapatali ndipo sangalole kuti chikhulupiriro chawo chiwonongeke.

Kodi tingatengere bwanji chitsanzo cha Yehova pa nkhani yoganizira anthu omwe akuzunzidwa?

Kodi tingapeze kuti nkhani zonena za a Mboni za Yehova omwe ali m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo?

Kodi panopo ndi abale ndi alongo angati amene ali m’ndende?