10:25-37

Yesu ananena fanizoli pamene ankayankha funso lakuti, “Nanga mnzanga amene ndikuyenera kumukonda ndani kwenikweni?” (Luka 10:25-29) Iye ankadziwa kuti mpingo wachikhristu udzapangidwa ndi anthu “osiyanasiyana” kuphatikizapo Asamariya komanso anthu a mitundu ina. (Yoh. 12:32) Fanizoli linathandiza otsatira ake kuti aziyesetsa kuchita zonse zomwe angathe kuti azikonda ena, ngakhale omwe amasiyana nawo m’zinthu zambiri.

DZIFUNSENI KUTI:

  • ‘Kodi ndimawaona bwanji abale ndi alongo a zikhalidwe zina?’

  • ‘Kodi ndimakonda kucheza ndi anthu okhawo omwe ndimafanana nawo m’zinthu zambiri?’

  • ‘Kodi pali zimene ndingachite kuti ndidziwane bwino ndi Akhristu ochokera m’mayiko ena komanso zikhalidwe zosiyanasiyana?’ (2 Akor. 6:13)

Kod ndi ndani amene ndikufuna kuti . . .

  •  adzalowe nane mu utumiki?

  •  abwere kudzadya kunyumba kwathu?

  •  abwere kwathu kudzachita nawo Kulambira kwa Pabanja?