Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mumadziimbabe Mlandu Yehova Akakukhululukirani?

Kodi Mumadziimbabe Mlandu Yehova Akakukhululukirani?

Nthawi zina zingakhale zovuta kuti tisiye kudziimba mlandu pa zoipa zimene tinachita ngakhale kuti Yehova anatikhululukira. Pamsonkhano Wachigawo wa 2016, womwe unali ndi mutu wakuti, “Pitirizani Kukhala Okhulupirika kwa Yehova,” panali nkhani komanso vidiyo yofotokoza za nkhaniyi. Gwiritsani ntchito pulogalamu ya JW Library kuti muonerenso vidiyoyi ndipo yankhani mafunso otsatirawa:

  • Kodi Sonia anakhala ali wochotsedwa kwa zaka zingati?

  • Kodi akulu anamuwerengera lemba liti, nanga linamuthandiza bwanji?

  • Kodi anthu a mumpingo anatani Sonia atabwerezeretsedwa?

  • Kodi Sonia ankavutika ndi maganizo otani, nanga bambo ake anamuthandiza bwanji?