Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Akulalikira kunyumba ndi nyumba ku Italy

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU July 2017

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za ulaliki wa Nsanja ya Olonda ndiponso kuphunzitsa choonadi chokhudza mavuto amene ali padzikoli. Gwiritsani ntchito zitsanzozi kuti mupange ulaliki wanuwanu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Kodi Muli ndi Mtima Wofewa Ngati Mnofu?

Kodi mtima wathu umakhudza bwanji zimene timasankha pa nkhani yokhudza zosangalatsa kapena kuvala ndi kudzikongoletsa? Kodi kukhala ndi mtima wofewa ngati mnofu kukutanthauza chiyani?

KUFUFUZA MFUNDO ZOTHANDIZA

Kodi Mumakwaniritsa Zimene Mwalonjeza?

Kodi tikuphunzira chiyani kwa Mfumu Zedekiya pa zimene anakumana nazo chifukwa choswa pangano?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Kodi Yehova Akatikhululukira Machimo, Amawakumbukirabe?

Kodi ndi zitsanzo ziti za m’Baibulo zimene zimasonyeza kuti Yehova amakhululukadi? Kodi zimene Yehova anachita ndi Davide, Manase komanso Petulo zimatithandiza bwanji kukhululupirira kuti nafenso akhoza kutikhululukira?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mumadziimbabe Mlandu Yehova Akakukhululukirani?

Nthawi zina zimakhala zovuta kuti tisiye kukumbukira zimene tinalakwitsa m’mbuyomo ngakhale kuti Mulungu anatikhululukira. Koma kodi n’chiyani chingatithandize?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Ufumu Unaperekedwa kwa Amene Ndi Woyenerera Mwalamulo

Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji ulosi wa Eziekieli wonena za mfumu yoikidwa mwalamulo? Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tizisonyeza Ulemu Tikafika Pakhomo

Tikafika pakhomo sitingadziwe ngati mwininyumba akutiona kapena akumvetsera zimene tikukambirana. Ndiye kodi tingatani kuti tizisonyeza ulemu?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Ulosi Wonena za Kuwonongedwa kwa Turo Umatithandiza Kuti Tizikhulupirira Kwambiri Mawu a Yehova

Ulosi wa Ezekieli wonena za kuwonongedwa kwa Turo unakwaniritsidwa mochititsa chidwi.